Psalms 93

1Yehova akulamulira, wavala ulemerero;
Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu,
dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
2Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale;
Inu ndinu wamuyaya.

3Nyanja zakweza Inu Yehova,
nyanja zakweza mawu ake;
nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.
4Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri,
ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja,
Yehova mmwamba ndi wamphamvu.

5Malamulo anu Yehova ndi osasinthika;
chiyero chimakongoletsa nyumba yanu
mpaka muyaya.
Copyright information for NyaCCL